Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 20:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namcitira cipongwe, nambweza, wopanda kanthu.

12. Ndipo anatumizanso wina wacitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja.

13. Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzacita ciani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamcitira iye ulemu.

14. Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzace, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti colowa cace cikhale cathu.

15. Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha, Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawacitira ciani?

16. iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iail

17. Koma iye anawapenyetsa iwo, nati, Nciani ici cinalembedwa,Mwala umene anaukana omanga nyumba,Womwewu unakhala mutu wa pangondya.

18. Munthu yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.

19. Ndipo alembi ndi ansembe akuru anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.

20. Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ace, kotero kuti akampereke iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.

21. Ndipo anamfunsa iye, nanena, Mphunzitisi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;

22. kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?

Werengani mutu wathunthu Luka 20