40. Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.
41. Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.
42. Ndipo pamene iye anakhala ndi zaka zace khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga macitidwe a phwando;
43. ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;
44. koma iwo anayesa kuti iye ali m'cipiringu ca ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;
45. ndipo pamene sanampeza, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna iye.
46. Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza iye m'Kacisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.
47. Ndipo 4 onse amene anamva iye anadabwa ndi cidziwitso cace, ndi mayankho ace.