Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 2:38-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.

39. Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa cilamulo ca Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mudzi kwao, ku Nazarete.

40. Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.

41. Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.

42. Ndipo pamene iye anakhala ndi zaka zace khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga macitidwe a phwando;

43. ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;

44. koma iwo anayesa kuti iye ali m'cipiringu ca ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao;

45. ndipo pamene sanampeza, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna iye.

46. Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza iye m'Kacisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.

47. Ndipo 4 onse amene anamva iye anadabwa ndi cidziwitso cace, ndi mayankho ace.

48. Ndipo m'mene anamuona iye, anadabwa; ndipo amace anati kwa iye, Mwanawe, wacitiranji ife cotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.

49. Ndipo iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine 5 ndikhale m'zace za Atate wanga?

50. Ndipo 6 sanadziwitsa mau amene iye analankhula nao.

51. Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo 7 amace anasunga zinthu izi zonse mumtima mwace.

52. Ndipo Yesu 8 anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'cisomo ca pa Mulungu ndi ca pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Luka 2