Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 2:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linaturuka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;

2. ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya.

3. Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu ali yense ku mudzi wace.

4. Ndipo Yosefe yemwe anakwera kucokera ku Galileya, ku mudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, ku mudzi wa Davine, dzina lace Betelehemu, cifukwa iye anali wa banja ndi pfuko lace la Davine;

5. kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati,

6. Ndipo panali pokhaia iwo komweko, masiku ace a kubala anakwanira.

7. Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

8. Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.

Werengani mutu wathunthu Luka 2