Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.