Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 19:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pamenepo: anati, Munthu wa pfuko lomveka ananka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.

13. Ndipo anaitana akapolo ace khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Cita nazoni malonda kufikira ndibweranso.

14. Koma mfulu za pamudzi pace zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu.

15. Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pocita malonda.

16. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu inacita nionjeza ndalama khumi.

17. Ndipo anati kwa iye, Cabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'cacing'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.

18. Ndipo anadza waciwiri, nanena, Mbuye, ndalama yanu yapindula ndalama zisanu.

19. Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu.

20. Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi ndalama yanu, ndaisunga m'kansaru;

21. pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula cimene simunaciika pansi, mututa cimene simunacifesa.

22. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula cimene sindinaciika, ndi wotuta cimene sindinacifesa;

Werengani mutu wathunthu Luka 19