Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 19:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo pakumva izi iwo, iye anaonjeza nanena fanizo, cifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.

12. Pamenepo: anati, Munthu wa pfuko lomveka ananka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.

13. Ndipo anaitana akapolo ace khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Cita nazoni malonda kufikira ndibweranso.

14. Koma mfulu za pamudzi pace zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu.

15. Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pocita malonda.

16. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu inacita nionjeza ndalama khumi.

17. Ndipo anati kwa iye, Cabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'cacing'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.

Werengani mutu wathunthu Luka 19