Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 19:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo analowa, napyola pa Yeriko. Ndipo taonani, mwamuna wochedwa dzina lace Zakeyu;

2. ndipo Iye anali mkulu wa amisonkho, nali wacuma.

3. Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sana the, cifukwa ca khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.

4. Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona iye; pakuti anati apite njira yomweyi.

5. Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.

6. Ndipo anafulumira, natsika, namlandira iye wokondwera.

7. Ndipo m'mene anaciona anadandaula onse, nanena, Analowa amcereze munthu ali wocimwa.

8. Ndipo Zakeyu anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.

9. Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero cipulumutso cagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.

10. Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa, cotayikaco.

11. Ndipo pakumva izi iwo, iye anaonjeza nanena fanizo, cifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.

Werengani mutu wathunthu Luka 19