Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:9-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

10. Anthu awiri anakwera kunka kukacisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzace wamsonkho.

11. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, acigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;

12. ndisala cakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi lamagawo khumi la zonse ndiri nazo.

13. Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafuna kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pacifuwa pace nanena, Mulungu, mundicitire cifundo, ine wocimwa.

14. Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwace woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzacepetsedwa; koma wodzicepetsa yekha adzakulitsidwa.

15. Ndipo anadzanao kwa iye ana amakanda kuti awakbudze; koma pamene ophunzira anaona, anawadzudzula.

16. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uti wa otere.

17. Indetu ndinena kwa inu, Ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

18. Ndipo mkuru wina anamfunsa iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizicita ciani, kuti ndilowe moyo wosatha?

19. Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.

20. Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

21. Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.

22. Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

23. Koma pakumva izi anagwidwa naco cisoni cambiri; pakuti anali mwini cuma cambiri.

24. Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

Werengani mutu wathunthu Luka 18