Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:32-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamcitira cipongwe, nadzamthira malobvu; ndipo atamkwapula adzamupha iye;

33. ndipo tsiku lacitatu adzauka.

34. Ndipo sanadziwitsa kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikira zonenedwazo.

35. Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha;

36. ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, ici nciani?

37. Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.

38. Ndipo anapfuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.

39. Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale cete; koma iye anapfuulitsa cipfuulire, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.

40. Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa iye: ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye,

41. Of una ndikucitire ciani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso.

42. Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.

Werengani mutu wathunthu Luka 18