Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa?

27. Koma iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

28. Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.

29. Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akumbala, kapena ana, cifukwa ca Ufumu wa Mulungu,

30. koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi yino; ndipo m'nthawi irinkudza moyo wosatha.

31. Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunkaku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.

32. Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamcitira cipongwe, nadzamthira malobvu; ndipo atamkwapula adzamupha iye;

33. ndipo tsiku lacitatu adzauka.

34. Ndipo sanadziwitsa kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikira zonenedwazo.

35. Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha;

36. ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, ici nciani?

37. Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.

Werengani mutu wathunthu Luka 18