Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uti wa otere.

17. Indetu ndinena kwa inu, Ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

18. Ndipo mkuru wina anamfunsa iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizicita ciani, kuti ndilowe moyo wosatha?

19. Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.

20. Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

21. Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.

22. Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

23. Koma pakumva izi anagwidwa naco cisoni cambiri; pakuti anali mwini cuma cambiri.

24. Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

Werengani mutu wathunthu Luka 18