Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 17:26-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.

27. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'cingalawa, ndipo cinadza cigumula, niciwaononga onsewo.

28. Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;

29. koma tsiku limene Loti anaturuka m'Sodoma udabvumba mota ndi sulfure zocokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;

30. momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu.

31. Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ace m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zace za m'mbuyo.

32. Kumbukilani mkazi wa Loti,

33. iye ali yense akafuna kusunga moyo wace adzautaya, koma iye ali yense akautaya, adzausunga.

34. Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

35. Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. [

36. ]

37. Ndipo anayankha nanena kwa iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.

Werengani mutu wathunthu Luka 17