Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 17:17-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwa khumi? koma ali kuti asanu ndi anai aja?

18. Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?

19. Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.

20. Ndipo pamene Afarisi anamfunsa iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayarikha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;

21. ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.

22. Ndipo anati kwa ophunzira ace, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona.

23. Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! taonani ili! musacoka kapena kuwatsata;

24. pakuti monga mphezi ing'anipa kucokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m'tsiku lace.

25. Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanizidwe ndi mbadwo uno.

26. Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.

27. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'cingalawa, ndipo cinadza cigumula, niciwaononga onsewo.

28. Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;

29. koma tsiku limene Loti anaturuka m'Sodoma udabvumba mota ndi sulfure zocokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;

30. momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu.

31. Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ace m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zace za m'mbuyo.

32. Kumbukilani mkazi wa Loti,

33. iye ali yense akafuna kusunga moyo wace adzautaya, koma iye ali yense akautaya, adzausunga.

34. Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

35. Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. [

Werengani mutu wathunthu Luka 17