Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 16:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.

27. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume ku nyumba ya atate wanga;

28. pakuti ndirinao abale asanu; awacitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ana a mazunzo.

29. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.

30. Koma anati, lai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wocokera kwa akufa adzasandulika mtima.

31. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Werengani mutu wathunthu Luka 16