Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 15:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo pakupita masiku owerengekamwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wace ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza cuma cace ndi makhalidwe a citayiko.

14. Ndipo pamene anatha zace zonse, panakhala njala yaikuru m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.

15. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwace kukaweta nkhumba.

16. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yace ndi makoko amene nkhumba rimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.

17. Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

18. Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena nave, Atate, ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu;

19. sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa anchito anu.

20. Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.

21. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.

22. Koma atateyo ananena kwaakapolo ace, Turutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni phete ku dzanja lace ndi nsapato ku apazi ace;

Werengani mutu wathunthu Luka 15