Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 15:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma amisonkho onse ndi anthu ocimwa analikumyandikira kudzamva iye.

2. Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ocimwa, nadya nao.

3. Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena,

4. Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'cipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

5. Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ace wokondwera.

6. Ndipo pakufika kunyumba kwace amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena nao, Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

7. Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

8. Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yace, nafunafuna cisamalire kufikira akaipeza?

9. Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena; Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.

10. Comweco, ndinena kwa inu, kuli cimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu cifukwa ca munthu wocimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Werengani mutu wathunthu Luka 15