Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 13:33-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkuca, cifukwa sikuloleka kuti mneneri aonongeke kunja kwace kwa Yerusalemu.

34. Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! ha! kawiri kawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ace m'mapiko ace, ndipo simunafunai!

35. onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Werengani mutu wathunthu Luka 13