Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:55-59 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

55. Ndipo pamene mphepo ya kumwela iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56. Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengoyino?

57. Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

58. Pakuti 8 pamene ulikupita naye mnzako wa miandu kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, ndi msilikari angaponye iwe m'nyumba yandende.

59. Ine ndinena kwa iwe, 9 Sudzaturukamo konse kufikira utalipira kakobiri kakumariza.

Werengani mutu wathunthu Luka 12