Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.

10. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

11. Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wace akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?

12. kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa cinkhanira?

13. Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha iye?

14. Ndipo analikuturutsa ciwanda cosalankhula. Ndipo kunali, citaturuka ciwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15. Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mkuru wa ziwanda amaturutsa ziwanda.

16. Koma ena anamuyesa, nafuna kwa iye cizindikilo cocokera Kumwamba.

17. Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.

18. Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.

Werengani mutu wathunthu Luka 11