Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:36-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lace lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwace ikuunikira iwe.

37. Ndipo pakulankhula iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.

38. Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba cakudya asanasambe.

39. Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.

40. Opusa inu, kodi iye wopanga kunja kwace sanapanganso m'kati mwace?

41. koma patsani mphatso yacifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse ziri zoyera kwa inu.

42. Koma tsoka inu, Afarisi! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa cakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka ciweruziro ndi cikondi ca Mulungu; mwenzi mutacita izi, ndi kusasiya zinazo.

43. Tsoka inu, Afarisi! cifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kulankhulidwa m'misika.

44. Tsoka inu! cifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa,

45. Ndipo mmodzi wa acilamulo anayankha, nanena kwa iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

46. Ndipo anati, Tsoka inunso, acilamulo inul cifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi cala canu cimodzi.

47. Tsoka inu! cifukwamumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.

Werengani mutu wathunthu Luka 11