Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pakukhala iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ace anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ace.

2. Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze;

3. tipatseni ife tsiku ndi tsiku cakudya ca patsiku.

4. Ndipo mutikhululukire ife macimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.

5. Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lace, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;

6. popeza wandidzera bwenzi langa locokera paulendo, ndipo ndiribe compatsa;

7. ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandibvuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa?

8. Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, cifukwa ali bwenzi lacevkoma cifukwa ca liuma lace adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azisowa.

Werengani mutu wathunthu Luka 11