Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 10:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana iye amene anandituma Ine.

17. Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.

18. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wocokera kumwamba.

19. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iri yonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.

20. Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.

21. Nthawi yomweyo iye anakondwera ndi Mzimu Wovera, nati, Ndikubvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

Werengani mutu wathunthu Luka 10