Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 9:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso masoka awiri m'tsogolomo.

13. Ndipo mngelo wacisanu ndi cimodzi anaomba, ndipo ndinamva mau ocokera ku nyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu,

14. nanena kwa mngelo wacisanu ndi cimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pa mtsinje waukuru Pirate.

15. Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi caka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.

16. Ndipo ciwerengero ca nkhondo za apakavalo ndico zikwi makumi awiri zocurukitsa zikwi khumi; ndinamva ciwerengero cao.

17. Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulfure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao muturuka moto ndi utsi ndi sulfure.

18. Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulfure, zoturuka m'kamwa mwao.

19. Pakuti mphamvu ya akavalo in m'kamwa mwao, ndi m'micira yao; pakuti micira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo.

20. Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa nchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolidi, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi amwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;

21. ndipo sanalapa mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena cigololo cao, kapena umbala wao.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 9