Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 6:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ndinaona pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi cimodzi, ndipo panali cibvomezi cacikuru; ndi dzuwa lidada bii longa ciguduli ca ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;

13. ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zace zosapsya, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.

14. Ndipo kumwamba kudacoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kucoka m'malo mwao.

15. Ndipo mafumu a dziko, ndi akuru, ndi akazembe, ndi acuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;

16. nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya iye amene akhala pa mpando wacifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa;

17. cifukwa lafika tsiku lalikuru la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 6