Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 6:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.

12. Ndipo ndinaona pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi cimodzi, ndipo panali cibvomezi cacikuru; ndi dzuwa lidada bii longa ciguduli ca ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;

13. ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zace zosapsya, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.

14. Ndipo kumwamba kudacoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kucoka m'malo mwao.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 6