Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 6:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula cimodzi ca zizindikilo zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva cimodzi mwa zamoyo zinai, nicinena, ngati mau a bingu, Idza.

2. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anaturukira wolakika kuti alakike.

3. Ndipo pamene anamasula cizindikilo caciwiri, ndinamva camoyo caciwiri nicinena, Idza.

4. Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.

5. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacitatu, ndinamva camoyo cacitatu nicinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lace.

6. Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.

7. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacinai, ndinamva mau a camoyo cacinai nicinena, Idza.

8. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.

9. Ndipo pamene adamasula cizindikilo cacisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa cifukwa ca mau a Mulungu, ndi cifukwa ca umboni umene anali nao:

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 6