Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 6:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula cimodzi ca zizindikilo zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva cimodzi mwa zamoyo zinai, nicinena, ngati mau a bingu, Idza.

2. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anaturukira wolakika kuti alakike.

3. Ndipo pamene anamasula cizindikilo caciwiri, ndinamva camoyo caciwiri nicinena, Idza.

4. Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.

5. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacitatu, ndinamva camoyo cacitatu nicinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lace.

6. Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.

7. Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacinai, ndinamva mau a camoyo cacinai nicinena, Idza.

8. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 6