Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 3:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

10. Popeza unasunga mau a cipiriro canga, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

11. Ndidza msanga; gwira cimene uli naco, kuti wina angalande korona wako.

12. Iye wakulakika, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kacisi wa Mulungu wanga, ndipo kuturuka sadzaturukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kucokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.

13. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

14. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikaya lemba:Izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa cilengo ca Mulungu:

15. Ndidziwa nchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

16. Kotero, popeza uti wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m'kamwa mwanga.

17. Cifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo cuma ndiri naco, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wocititsa cifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

18. ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m'moto, kuti ukakhale wacuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadzibveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

19. Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.

20. Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 3