Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 3:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kotero, popeza uti wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula m'kamwa mwanga.

17. Cifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo cuma ndiri naco, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wocititsa cifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;

18. ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyengeka m'moto, kuti ukakhale wacuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukadzibveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

19. Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero cita cangu, nutembenuke mtima.

20. Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

21. Iye wakulakika, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wacifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wacifumu wace.

22. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 3