Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 22:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wace kukaonetsera akapolo ace zimene ziyenera kucitika msanga.

7. Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a cinenero ca buku ili.

8. Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.

9. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usacite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.

10. Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza cizindikilo mau a cinenero ca buku ili; pakuti nthawi yayandikira.

11. Iye wakukhala wosalungama acitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama acitebe colungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.

12. Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa nchito yace.

13. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, ciyambi ndi citsiriziro.

14. Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.

15. Kunja kuli agaru ndi anyanga, ndi acigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulicita.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 22