Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 22:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa nchito yace.

13. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, ciyambi ndi citsiriziro.

14. Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.

15. Kunja kuli agaru ndi anyanga, ndi acigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulicita.

16. Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukucitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzo ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.

17. Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani, Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.

18. Ndicita umboni kwa munthu ali yense wakumva mau a cinenero ca buku ili, 1 Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu:

19. ndipo 2 ali yense akacotsako pa mau a buku la cinenero ici, Mulungu adzamcotsera gawo lace pa mtengo wa moyo, ndi 3 m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.

20. Iye wakucitira umboni izi, anena, 4 Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.

21. 5 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi oyera mtima onse, Amen.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 22