Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 20:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka cikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.

6. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.

7. Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;

8. nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja.

9. Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.

10. Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.

11. Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao.

12. Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao.

13. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,

14. Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.

15. Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 20