Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 20:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala naco cifungulo ca phompho, ndi unyolo waukuru m'dzanja lace.

2. Ndipo anagwira cinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka cikwi,

3. namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka cikwi; patsogolo pace ayenera kumasulidwa iye kanthawi.

4. Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.

5. Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka cikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.

6. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 20