Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 2:15-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Kotero uli nao akugwira ciphunzitso ca Anikolai momwemonso.

16. Cifukwa cace lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posacedwa, ndipo ndidzacita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.

17. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.

18. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba:Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ace ngati lawi la moto, ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira:

19. 1 Ndidziwa nchito zako, ndi cikondi, ndi cikhulupiriro, ndi utumiki, ndi cipiriro cako, ndi kuti nchito zako zotsiriza cicuruka koposa zoyambazo.

20. Komatu ndiri nako kotsutsana ndi iwe, cuti ulola mkazi 2 Yezebeli, wodzieha zekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa akapolo anga, kuti acite cigololo ndi kudya zoperekedwa nsenbe kwa mafano.

21. Ndipo ndanpatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana naco cigololo cace.

22. Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akucita cigololo naye kuwalonga m'cisautso cacikuru, ngati salapa iwo ndi kuleka nchito zace.

23. Ndipo ndidzaononga ana ace ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti 3 ine ndine iye amene ayesa imso ndi mitima; ndipo 4 ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa nchito zanu.

24. Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiyatira, onse amene alibe ciphunzitso ici, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.

25. Koma 5 cimene muli naco, gwirani kufikira ndikadza.

26. Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga nchito zanga kufikira citsiriziro, kwa iye 6 ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;

27. ndipo 7 adzawalamulira ndi ndodo yacitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga lnenso ndalandira kwa Atate wanga;

28. ndipo ndidzampatsa iye 8 nthanda.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 2