Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 17:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo cirombo cinalico, ndi kulibe, ico comwe nelieo cacisanu ndi citatu, ndipo ciri mwa zisanu ndi ziwirizo, nicimuka kucitayiko.

12. Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi cirombo.

13. Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa cirombo.

14. Iwo adzacita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, cifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.

15. Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wacigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.

16. Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi cirombo, izi zidzadana ndi mkazi wacigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yace, nizidzampsereza ndi moto.

17. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kucita za m'mtima mwace, ndi kucita ca mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa cirombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.

18. Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukuru, wakucita ufumu pa mafumu a dziko.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 17