Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 16:4-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo wacitatu anatsanulira mbale yace ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.

5. Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, cifukwa mudaweruza kotero;

6. popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 16