Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 10:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pace, ndi nkhope yace ngati dzuwa, ndi mapazi ace ngati mizati yamoto;

2. ndipo anali nako m'dzanja lace kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lace lamanja panyanja,

3. ndi Iamanzerelo pamtunda, napfuula ndi mau akuru, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anapfuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.

4. Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo udinamva mau ocokera Kumwamba nanena, Sindikiza naco cizindikilo zimene adalankhula mabingu asanu ndi limodzi, ndipo usazilembe,

5. Ndipo mngelo amene ndinamuona alikuimirira panyanja ndi pa mtunda, anakweza dzanja lace lamanja kuloza kumwamba,

6. nalumbira kuchula iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:

7. komatu m'masiku a mau a mngelo wacisanu ndi ciwiri m'mene iye adzayamba kuomba, pamenepo padzatsirizika cinsinsi ca Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ace aneneri.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 10