Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 1:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo pamene ndinamuona iye, ndinagwa pa mapazi ace ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lace lamanja pa ine, nati, Usaope, ine ndine woyamba ndi wotsiriza,

18. ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.

19. Cifukwa cace 2 lembera zimene unaziona, ndi zimene ziripo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;

20. 3 cinsinsi ca nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi 4 zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo 5 angelo a Mipingo isanu ndi iwirl; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo 6 Mipingo isanu ndi iwiri.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 1