17. Ndipo pamene ndinamuona iye, ndinagwa pa mapazi ace ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lace lamanja pa ine, nati, Usaope, ine ndine woyamba ndi wotsiriza,
18. ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.
19. Cifukwa cace 2 lembera zimene unaziona, ndi zimene ziripo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;