1. CIBVUMBULUTSO ca Yesu Kristu, cimene Mulungu anambvumbulutsira acionetsere akapolo ace, ndico ca izi ziyenera kucitika posacedwa: ndipo potuma mwa mngelo wace anazindikiritsa izi kwa kapolo wace Yohane;
2. amene anacita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Kristu, zonse zimene adaziona.