Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.

2. Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.

3. Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;

4. kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.

5. Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:

6. pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.

7. Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.

8. Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

9. Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.

10. Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 8