Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 7:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.

10. Ndipo lamulo, limene linali Iakupatsa moyo, ndinalipeza lakupassa imfa.

11. Pakuti ucimo, pamene unapeza cifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.

12. Cotero cilamulo ciri coyera, ndi cilangizo cace ncoyera, ndi colunaama, ndi cabwino.

13. Ndipo tsopano cabwino cija cinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma ucimo, kuti uoneke kuti uli ucimo, wandicitira imfa mwa cabwino cija; kuti ucimo ukakhale wocimwitsa ndithu mwa lamulo.

14. Pakuti tidziwa kuti cilamulo ciri cauzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa kapolo wa ucimo.

15. Pakuti cimene ndicita sindicidziwa; pakuti sindicita cimene ndifuna, koma cimene ndidana naco, ndicita ici.

16. Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, ndibvomerezana naco cilamulo kuti ciri cabwino.

17. Ndipo tsopano si ine ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.

18. Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza.

19. Pakuti cabwino cimene ndicifuna, sindicicita; koma coipa cimene sindicifuna, cimeneco ndicicita.

20. Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, si ndinenso amene ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.

21. Ndipo cotero odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko.

22. Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi cilamulo ca Mulungu:

23. koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m'ziwalo zanga.

24. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi?

25. Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 7