Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 7:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wace wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.

3. Ndipo cifukwa cace, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wace wamoyo, adzanenedwa mkazi wacigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; cotero sakhala wacigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

4. Cotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku cilamulo ndi thupi la Kristu; kuti mukakhale ace a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso,

5. Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za macimo, zimene zinali mwa cilamulo, zinalikucita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso,

6. Koma tsopano tinamasulidwa kucilamulo, popeza tinafa kwa ici cimene tinagwidwa naco kale; cotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'cilembo cakale ai.

7. Pamenepo tidzatani? Kodi cilamulo ciri ucimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira ucimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira cilakolako sicikadati cilamulo, Usasirire;

8. koma ucimo, pamene unapeza cifukwa, unacita m'kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo ucimo uli wakufa.

9. Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.

10. Ndipo lamulo, limene linali Iakupatsa moyo, ndinalipeza lakupassa imfa.

11. Pakuti ucimo, pamene unapeza cifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.

12. Cotero cilamulo ciri coyera, ndi cilangizo cace ncoyera, ndi colunaama, ndi cabwino.

13. Ndipo tsopano cabwino cija cinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma ucimo, kuti uoneke kuti uli ucimo, wandicitira imfa mwa cabwino cija; kuti ucimo ukakhale wocimwitsa ndithu mwa lamulo.

14. Pakuti tidziwa kuti cilamulo ciri cauzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa kapolo wa ucimo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 7