Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 7:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo licita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?

2. Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wace wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.

3. Ndipo cifukwa cace, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wace wamoyo, adzanenedwa mkazi wacigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; cotero sakhala wacigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

4. Cotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku cilamulo ndi thupi la Kristu; kuti mukakhale ace a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso,

5. Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za macimo, zimene zinali mwa cilamulo, zinalikucita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso,

Werengani mutu wathunthu Aroma 7