Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 6:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye;

9. podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye.

10. Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11. Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.

12. Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zace:

13. ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za cilungamo,

14. Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a cisomo.

Werengani mutu wathunthu Aroma 6