Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 6:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace tidzatani? Tidzakhalabe m'ucimo kodi, kuti cisomo cicuruke?

2. Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m'menemo?

3. Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?

4. Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.

5. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace;

6. podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo;

7. pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo.

8. Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye;

9. podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye.

10. Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11. Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.

12. Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zace:

Werengani mutu wathunthu Aroma 6