Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 5:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakucimwa, pakuti mlandu ndithu unacokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere icokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.

17. Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.

18. Cifukwa cace, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; comweconso mwa cilungamitso cimodzi cilungamo ca moyo cinafikira anthu onse.

19. Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ocimwa, comweco ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.

20. Ndipo lamulo linalowa moyenjezera, kuti kulakwa kukacuruke; koma rl pamene ucimo unacuruka, pomwepo cisomo cinacuruka koposa;

21. kuti, mongaucimo unacita ufumu muimfa, comweconso cisomo cikacite ufumu mwa cilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 5