Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 5:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti ngati, pokhala ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wace.

11. Ndipo si cotero cokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene talandira naye tsopano ciyanjanitso.

12. Cifukwa cace, monga ucimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse, cifukwa kuti onse anacimwa.

13. Pakuti kufikira nthawi ya lamulo ucimo unali m'dziko lapansi; koma ucimo suwerengedwa popanda lamulo.

14. Komatu imfa inacita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanacimwa monga macimwidwe ace a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.

15. Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa cifukwa ca kulakwa kwammodziyo, makamaka ndithu cisomo ca Mulungu, ndi mphatso yaulere zakucokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinacurukira anthu ambiri.

16. Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakucimwa, pakuti mlandu ndithu unacokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere icokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.

17. Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 5