Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 16:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.

19. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.

20. Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.

21. Timoteo wanchito mnzanga akulankhulani inu; ndi Lukiyo ndi Yasoni ndi Sosipatro, abale anga.

22. Ine Tertio, ndirikulemba kalata ameneyu, ndikulankhulani inu mwa Ambuye.

23. Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Eklesia yense wa Ambuye, akulankhulani inu. Erasto, ndiye woyang'anira mudzi, akulankhulani inu, ndiponso Kwarto mbaleyo.

25. Ndipo kwa iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa uthenga wanga wabwino, ndi kulalildra kwa Yesu Kristu, monga mwa bvumbulutso la cinsinsi cimene cinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,

26. komai caonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere cikhulupiriro;

27. kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu Aroma 16